jpeg

Gawo #332, June 19, 2024

Barnaba: Kutumikira Ndi Kupezeka Kwake

Imodzi mwa njira zopambana zomwe Barnaba anatumikilira mpingo oyamba inali kupezeka kwake basi. Kwa nthawi zingapo nkhani yake muli zitsanzo zomwe anatumizidwa ndi atsogoleri a mpingo kuti akwanilitse cholinga chapadela kumpingo watsopano wa ku Antiokea.

Machitidwe a Atumwi 11

22 Mbiri imeneyi inamveka ku mpingo wa ku Yerusalemu ndipo iwo anatumiza Barnaba ku Antiokeya. Kenako Barnaba anatumidwa kuti akapeleke mphatso ya ndalama.

Machitidwe a Atumwi 11

29 Ophunzirawo, aliyense monga mwakupata kwake, anatsimikiza kuthandiza abale okhala ku Yudeya. 30 Izi anazichitadi ndipo anatuma Barnaba ndi Saulo kukapereka mphatsozo kwa akulu a mpingo. Panthawi ina, monga taona kale, anatumidwa ndi Paulo pa ulendo oyamba okadzala mpingo.

Machitidwe a Atumwi 13

3 Ndipo atasala kudya ndi kupemphera anasanjika manja awo pa iwo nawatumiza. Pomwe oyendetsa madongosolo a mpingo adakumana kuti apange chisankho cha yemwe atumizidwe, Barnaba anasankhidwa pamodzi ndi ena, kukapereka zomwe anagwirizana ku mipingo ya anthu amitundu Ina.

Machitidwe a Atumwi 15

22 Pamenepo atumwi ndi akulu ampingo, pamodzi ndi mpingo onse, anagwirizana zosankha anthu ena pakati pawo kuti awatume ku Antiokeya pamodzi ndi Paulo ndi Bamaba. Iwo anasankha Yudasi, wotchedwa Barsaba ndi Sila, anthu awiri amene anali atsogoleri pakati pa abale, Kawilikawili timaganiza kuti ndi amene amayang'ana anthu oti awatume kukawalimbikitsa ntchito. Koma Barnaba akutionetsa kuti  atsogoleri muutumiki amapezeka kuti atumidwe. Mmene Iye analiri anali opezeka pomwe wafunikira ndi komwe wafunikira. Atsogoleri muutumiki amaphunzila kuchokela ku chitsanzo chake momwe angatumikilire pokhala opezeka.

Kupezeka kumatumikila ena posiya mapulogalamu ako

Barnaba anali opezeka kuti atumidwe ndi kumangotumidwabe kuti atumikire ena. Anapereka mphatso yamtengo wapatali ya mtsogoleri, nthawi! Akuyenela kuti anali ndi zake zoti achite asanatumidwe, koma anazisiya zimenezo kuti cholinga cha gulu chikwanilitsidwe. Atsogoleri muutumiki amayang'anira nthawi yawo mosamala koma amaphunzila kuchokela kwa Barnaba kuti asagwilitse nthawi yawo modzikonda. Amakhala ofuna kusiya mapulogalamu awo kuti chosowa Cha wina chikwanilitsidwe. Sakhumudwa kapena kunyozeka potumidwa. Amatumikira popezeka kwawo.

Kupezeka kumatumikila ena popereka zomwe zimakubweletsela phindu

Barnaba anali opezeka Kutumikira ndi mphatso komanso maluso omwe anabweretsa kugulu. Anali olimbikitsa ndipo anatumizidwa kukalimbikitsa. Anali wanzeru,ndipo anatumidwa kukapereka uthenga ofunikila. Anali odalirika, ndipo anatumizidwa kuti akalongosole bwino zokhuza ndalama. Anali wamaluso apamwamba ngati mtsogoleri, koma mwakufuna kwake amapereka mphatso zake kuti zikhalepo ndicholinga chotumikira gulu. Atsogoleri muutumiki amabweletsa mphatso zawo kuti zitumikire gulu, osati ndicholinga choti atamandidwe. Amapanga mphatso zawo kupezeka mmene zikufunikira ndi cholinga. Amatumikira pokhala opezeka.

Zoti tilingalire ndi kukambirana

  • Kodi kupezeka Kwa Barnaba kukundiphunzitsa chani ine ngati mtsogoleri? Kodi ndichite chani msabatayi kuti ndikhale monga Iyeyu?
  • Kodi ndine omasuka pa mapulogalamu anga kapena nthawi yanga kuti ndizikhala opezeka chifukwa cha zosowa ena? Kodi nditasintha pati mmene ndimayendetsela nthawi yanga kuti ndipeleke mwayi oti ndizipezeka?
  • Kodi ndimaona kuti maluso ndi maukadaulo omwe ndilinawo ngati zipangizo zoti ndizigwilitsa ntchito ndekha kapena chifukwa cha ena? Kodi ndingaoange bwanji kuti zipezeke mukutumikira ena?
  • Kodi ndine ofuna kupereka maloto anga ndi mapulani anga chifukwa cha ena? Kodi chimandivuta ndichani kuti ndipeleke mapulaniwa? Kodi nditsate ndondomeko ziti mu utsogoleri wangawu kuti ndisiye mapulani anga chifukwa cha gulu?

Mpaka nthawi Ina, ine wanu wapaulendo,

Jon Byler

Muphunziro lotsatirali, tiona momwe Barnaba anatumikilira ndi kudzichepetsa kwake.

Kuti muone maphunziro a m'buyomu, dinani apa.

Tumizani kwa anzanu omwe akufuna kutsatila chitsanzo cha Yesu potsogolera ngati otumikira. Angathe kulembetsa mwaulere komanso kuona magawo akale.mukafuna kupeza magawo akale, dinani apa. Magawo awa amatanthauziridwa mchichewa ndi abusa Grace Kacheto, gracekacheto@yahoo.com

Reflections for Serving Leaders is published by Center for Serving Leadership and Jon Byler. Copyright, 2024