Atsogoleri Muutumiki akhoza kuphunzira zochita zambiri kuchokela Kwa Barnaba zomwe zingawonjezele luso la utsogoleri wawo ndi kuthekela kwawo. Taonapo kale za Kutumikira kwake popeleka, polimbikitsa ndi kugwila ntchito kwake ngati gulu. Tikaonetsetsa nkhani yake ikuonetsela mmene chikhalidwe chake chiliri.
Machitidwe a Atumwi 13
1 Mu mpingo wa ku Antiokeya munali aneneri ndi aphunzitsi awa: Barnaba, Simeoni, Lukia wa ku Kurene, Manayeni (amene analeredwa pamodzi ndi mfumu Herode), ndiponso Saulo. 2 Iwo pamene ankapembedza Ambuye ndi kusala kudya, Mzimu Woyera anati, “Mundipatulire Barnaba ndi Saulo kuti akagwire ntchito imene ndinawayitanira.” 3 Ndipo atasala kudya ndi kupemphera anasanjika manja awo pa iwo nawatumiza.
Kodi Barnaba ndi gulu lake la atsogoleriwa amatani? Kodi amalingalira za mtsogolo? Kupanga ndondomeko ya zomwe azachite mu zaka zisanu zikubwela? kukhazikitsa ndandanda wa zinthu zoti achite kuti akwanilitse masomphenya amtsogolo? Pomwe zochitika zonsezi zili zoyenera, gulu limeneli "limapembedza Mulungu ndiponso kusala kudya..." Chitsanzo cha Barnaba chikuwonetsela momwe kupembedza kumasinthila atsogoleri muutumiki.
Kupembedza kumatumikila pa kusintha kwa mtima
Gulu limeneli la atsogoleri linasonkhana mu kupembedza. Mchitidwe wawo opembedza unali mwakufuna kwawo kuti chindunji chawo chikhale Cha kwa Mulungu. Anaika chindunji cha mitima ndi malingaliro awo pa Mulungu. Anasala chakudya ngati mchitidwe ozikaniza okha zomwe matupi awo amalakalaka. Kulambira kwawo kunasuntha kakhalidwe ka mitima yawo kutali ndi Iwo.Kupembedza kunasuntha chindunji chawo kuchoka pa iwo eni kufikila pa Mulungu.
Atsogoleri ambiri amaika chindunji kapena chidwi chawo pa zochitika kunja kwa utsogoleri ndipo zambiri zimachitika popanda kusintha kwa mtima. Koma zochitikazi zitha kukhala zozitumikira wekha pokhapokha patakhala kusintha kwa mtima. Kupembedza kumatulutsa kusintha kwa mtima. Kupembedza kunasuntha chidwi cha mtima kuchoka pa iwe, masomphenya athu, mapulani ndi maloto, ndikusitha mitima yathu kuloza kumwamba ndi kunja. Kusintha kwa mtimaku ndi kozungulira ndipo kumakonzekeletsa tsogoleri yemwe akutumikila kuti atumikire ena mosavuta. Zimapatsa kuthekela mtsogoleri kuti akhale ndi chindunji chake ku zakumwamba koposa pa chidwi cha iyemwini. Kupembedza kumawumba zolinga za mitima yathu ndipo kumapanga khalidwe. Mitima yathu ndiyofunika! khalidwe lathu ndiyofunika! Kusintha kwa mtima ndi kofunika kuti tikhale osadzikonda tokha zomwe utsogoleri otumikila umafuna. Utsogeri weniweni otumikila anthu umayamba ndi mtima osinthika pomwe wakumana ndi Mulungu.
Kupembedza kumatumikila posintha mutu
Munthawi yomwe gulu limeneli linkapembedza, anamva chitsogozo chomveka bwino cha Mzimu Oyera. Popanda kupembedza kapena kulambira, akanatha kuika chidwi cha malingaliro awo polimbikitsa mpingo omwe unalipo kale ku Antiokea. Koma popembedza amapezeka kuti asintha maganizo awo ndi chindunji chawo. Kulambira kumabweletsa kusintha kwa maganizo. Atsogoleri ambiri amayesetsa kusintha kuganiza kwawo kuti akhale mtsogoleri opambana. Koma atsogoleri muutumiki amazindikira kuti kupembedza kumasintha kuganiza kwawo mofunikira.
Kupembedza kumatumikila posinthana manja
Atamvetsela malangizo a Mzimu Oyera, gulu linaika manja pa Barnaba ndi Saulo ndikuwatumiza. Lingalirani kupambana kwa nchitidwewu. Awiriwa anali atsogoleri akulu akulu ampingo ndipo tsopano awachotsa nkuwatumiza kwinakwake! Izi zinali zadzidzidzi ndi zosayembekezeka. Kupembedza kumatulutsa kusintha kwa kachitidwe kazinthu. Atsogoleri muutumiki amalolera Mulungu awatsogolere mu njira zatsopano pomwe akupembedza. Mitima ndi mitu zomwe ndi zosinthika zotsatila zake ndi kusintha kwa zochitika zomwe zili mmanja . Machitidwe enieni a utsogoleri amatuluka mu kupembedza. |