jpeg

Gawo #329, May 8, 2024

Barnaba: Kutumikila Popeleka Moolowa Manja

Chinthu choyamba chomwe chimene Barnaba anachita chomwe chinalembedwa ndi chimodzi mwa zopereka zake zopambana.

Machitidwe a Atumwi 4

36 Yosefe, wa fuko la Levi, wochokera ku Kupro amene atumwi anamutcha Barnaba, kutanthauza kuti mwana wachilimbikitso, 37 anagulitsa munda wake ndipo anadzapereka ndalamazo kwa atumwi.

Barnaba anagulitsa munda omwe unali wake ndikupeleka  ndalama zonse kwa atsogoleri a mpingo. Iyeyu sanali oyamba wa okhulupilira kupanga izi (Onani pa Machitidwe 4:34), koma dzina lake ndi loyamba kutchulidwa atapanga zimenezi. Machitidwe ake akuonetsa kuti ndi omwe anatakasa Hananiya ndi Safira kuti nawonso agulitse malo awo (Onani pa Machitidwe 5:1-11). Koma mtima wawo ndi zolinga zawo zinali zosemphana kutali ndi za Barnaba. Kupeleka moolowa Manja kwa Barnaba kukuonetsela njila zomwe atsogoleri onse muutumiki akuchita bwino kutsatila.

Kupereka moolowa manja kumatumikila poonetsela kupereka nsembe.

Barnaba anagulitsa munda wake. Mundawu ukuyenela kuti unali kwawo ku Cypras ndipo mwinanso unali cholowa cha kubanja kwake. Akuyenela kuti anachita kupanga ulendo wa kwawo kenaka atagulitsa nkubweletsa ndalamazo ku Yerusalem. Mulimonsemo,pamwamba popeleka ndalama zonse zamundawo anapelekanso nthawi ndi mphamvu zake. Mchitidwe wake opereka moolowa manja unali nsembe ndipo unapereka chithunzi cha mtima wake opereka. Atsogoleri ambiri ali pa maudindo a utsogoleri chifukwa cha zomwe angapeze monga ndalama, kutchuka kapena mphamvu.

Koma atsogoleri otumikila amapeleka zokhumba zawo ndi zosowa zawo kuti atumikile Iwo amene akuwatsogolera. Nthawi zina,monga Barnaba, izi zitha kukhala nsembe yandalama. Koma nthawi zambiri, atsogoleri muutumiki amapereka nsembe nthawi ndi mphamvu, kapena zinthu zina zofunikira kwa omwe akuwatsatira. Kupereka koolowa manja kwenikweni nthawi zonse kumafuna nsembe yamtengo wapamwamba.

Kupereka moolowa manja kumatumikila poonetsela kukhudzika.

Barnaba anasunthika nkupereka chifukwa cha zosowa za mudela. Munali anthu omwe anali ndi zosowa ndipo anali ndi kukhudzika ndi chisoni kwa Iwo. Sanali kuonela ena pansi, koma anali kuyang'ana kuti afikile ndani. Mchitidwe wake opereka moolowa manja ukuonetsela mtima wake wokhudzika ndi zosowa za ena kuposa zosowa zake. Anazindikila kuti anali ndi katundu yemwe cholinga chake sichinali choti agwilitse ntchito Iye yekha koma kuti adalitse enanso.

Atsogoleri ambiri amaona ena ngati njila yothela, anthu omwe angathandize kukwanilitsa masomphenya ndi cholinga cha bungwe. Koma atsogoleri muutumiki samaona 'antchito' kapena 'mamembala' koma amaona anthu okhala ndi maloto awo, za pamtima pawo ndi zokhumba zawo. Amaika maso awo pa ena ndi kuona mwai oti adalitse ndi kulimbikitsa. Chifukwa choti atsogoleri muutumiki amaika chindunji cha mtima wawo kunja, amatha kuchitapo kanthu pa zosowazi ndi kukhuzika komanso chifundo. Amazindikila kuti anapatsidwa mphatso ndi zinthu zomwe cholinga chake ndi choti zifikile mwa iwo kenaka zipitilile Kwa ena .

Atsogoleri muutumiki amapereka moolowa manja kwa iwo amene ali ndi zosowa zenizeni chifukwa amasamaladi za ena ndipo amakhudzika ndi zosowa zawo.

Kupereka moolowa manja kumatumikila pozikaniza wekha

Barnaba anagulitsa munda wake "ndikubweletsa ndalama ndikuziika pamapazi a atumwi". Pochita izi anazikaniza ufulu otsata ndalama zomwe anapelekazo kuti zagwila ntchito motani. Atumwi ndi omwe amadziwa zochita nazo ndalama zopelekedwazo mumpingo oyamba. Sanali opereka kuti alandile matamando. Pomwe mwachilengedwe timafuna tizindikilike ndi ena pa ntchito zabwino zomwe tachita, Barnaba anazikaniza yekha ku izi. Mchitidwe wake opereka moolowa manja ukuonetsela chomwe chili mumtima mwake chomwe chinali Cha pa ena osati Cha pa iyemwini.

Atsogoleri ambiri amafuna kukhala opereka ngati Barnaba koma koma amafuna kuonetsetsa kuti dzina lawo lalengezedwa pa ndandanda wa anthu othandiza. Ena amapereka moolowa manja koma amafuna alamulire ndalamazo zikamatuluka kapena kunena njila zomwe akufuna pa  mphatso zawozo kuti zilandilidwe motani. Koma atsogoleri muutumiki amazikaniza okha  ndipo moolowa manja amapereka mphamvu Kwa ena.

Zoti tilingalire ndi kukambirana

  • Kodi kupereka kwa Barnaba kukundionetsela bwanji ine ngati mtsogoleri? Kodi ndingachite chani msabatayi kuti ndikhale monga  iyeyo?
  • Ndikamapereka, kodi kupereka kwanga ndi kwansembe kapena ndimangopereka chomwe chilibe ntchito kwa ine kapena chomwe sindigwilitsa ntchito munjila iliyonse? Kodi nditsate ndondomeko ziti kuti ndizipereka moolowa manja?
  • Kodi ndimawaona bwanji ena omwe ali mugulu langa? Kodi ndimawaona ngati anthu omwe alipo kuti andithandize kukwanilitsa masomphenya anga kapena ngati anthu omwe ali ofanana ndi ine, okhala ndi maloto awo, zokhumba komanso zovuta zawo? Kodi maonedwe anga pa ena akukhudza bwanji utsogoleri wanga?
  • Lingalirani nthawi yomwe munaperekapo chuma kapena zinthu Kwa ena ndi mafunso amenewa. Kodi ndinatha kupereka popanda kufuna kulengezedwa kapena kuyamikiridwa? Kodi ndinatha kupereka ulamuliro pa mphatso yanga  kwathunthu Kwa olandilayo kapena ndinali ndi mphamvu pa zochitikazo? Kodi machitidwe anga akuonetsela chani za mtima wanga ?
  • Werengani Machitidwe 5:1-11, nkhani ya Hananiya ndi Safira omwe nawonso anagulitsa munda wawo.Kodi kupereka kwawo kukusiyana bwanji ndi kwa Barnaba?

 

Mpaka nthawi Ina, ine wanu wapaulendo,

Jon Byler

Muphunziro lotsatirali, tiona momwe Barnaba anatumikilira ndi gulu.

Kuti muone maphunziro a m'buyomu, dinani apa.

Tumizani kwa anzanu omwe akufuna kutsatila chitsanzo cha Yesu potsogolera ngati otumikira. Angathe kulembetsa mwaulere komanso kuona magawo akale.mukafuna kupeza magawo akale, dinani apa. Magawo awa amatanthauziridwa mchichewa ndi abusa Grace Kacheto, gracekacheto@yahoo.com

Reflections for Serving Leaders is published by Center for Serving Leadership and Jon Byler. Copyright, 2024