Mawu a Mulungu anali okongola ndipo opanda cholakwika! Mauwo anali odzala ndi zonse zokometsela zomwe zikapeleka danga loti dzikolapansi lokoma lipitilire kwa mibadwo. Ndiye,pomwe Mulungu walenga dzikolapansi lopanda koipa kalikonse ndinso la mkaka ndi uchi, Sanaleke kuliyang'anila chifukwa cha Kulephela kwa Adamu ndi Eva! Pomwe anatembelera njoka, anaonetsela mapulani ake a chigonjetso chachikulu, zaka zikwi zikwi zisanachitike.
Genesis 3
15 Ndipo ndidzayika chidani pakati pa iwe ndi mkaziyo, pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake; Iye adzaphwanya mutu wako ndipo iwe udzaluma chidendene chake.
Kenaka, atatembelera njoka ndi nthaka, Mulungu akupitiliza kuchitapo kanthu potsatila kusamvela Kwa Adamu ndi Eva. Chinanso, Mulungu akuonetsa kuti sanali odabwa ndi mmene Adamu ndi Eva anachitila.
Genesis 3
21 Yehova Mulungu anapangira Adamu ndi mkazi wake zovala zachikopa ndipo anawaveka.
Mulungu mwachisomo anapeleka zovala za chikopa kwa Adamu ndi Eva; zolimba kuposa masamba chabe amene anagwilitsa ntchito podziphimba okha. Koma andaika malire atsopano mmalo mwake ndi kupeleka uphungu watsopano Oti Adamu agwile ntchito kunja kwa munda okongola ndi wabwino kukhala uja.
Kudziwilatu Kulephela kumabweletsa kukoma pozindikila cholinga
Poti Mulungu analibe cholinga choti banja loyamba lilephele, anadziwilatu ndipo anakonzeka pa za zomwe zinachitikazo. Sanawasiye choncho pa zotsatila za tchimo lawo, koma anakatha kupeleka zoti achite kwa iwo zitatha izi. Cholinga cha Mulungu pa iwo atagwa chinali choti iwo akhale mwathunthu mmene akanathela mudziko lokoma. Anali okonzeka kuwathandiza apite chitsogolo posatengela Kulephela kwawo.
Mudziko lathu lophwasukali, titha ndithu kudziwa za Kulephela kawilikawili! Kudziwilatu Kulephela sikutanthauza kuti kuona kulephelako pa chochitika chilichonse, koma zikuthanthauza kuti kuganiza kopita patsogolo polingalira ndondomeko zomwe zingatsatidwe pomwe kulephela kwachitika. Atsogoleri muutumiki amaphunzila kuti ndibwino kukonzekela kulephela koposa kudzidzimuka zikachitika!
Kudziwilatu Kulephela kumabweletsa kukoma pozindikila zotsatila
Kuchokela pa Kulephela kwa Adamu ndi Eva, takhala ndi maumwayi ambilimbili ophunzila pa kulephela! Koma kawilikawili timakhala odabwa ndi nkhani za atsogoleri omwe agwidwa mu mchitidwe osakhalabwino ndikuwachotsa pomwe chinachake sichinayende momwe zimafunikila.
Ena amakhala amanyazi ndi mantha. Amaopa zotsatila, chilango,ndi manyazi a kulephela kwawo ndipo amaphimba kulephelako, kukana kapena kukuthawa.
Ena akalephela amangozitenga olephela nthawi zonse. Mmalo monena chonchi, " ndinalephela" amavomela chonchi "ndine olephela". Kuvomela ngati uku sikupeleka kupindula komwe kumabwela patsogolo pake.
Koma atsogoleri otumikila amaphunzila kudziwilatu kulephela ndipo amakonzekela bwino lomwe. Akamapanga motele, magulu awo atha kupita patsogolo ndikuchitabwino. Mmalo mwa mantha akalephela muzalowa kulakalaka kuvomeleza chenicheni cha kulephela ndi kuchigwilitsa ntchito ngati mbali ya ulendo ophunzila. Atsogoleri muutumiki amakumbitsa magulu awo kuti ngakhale atalephela, kulephela si iwowo! atsogoleri otumikila amadziwilatu kuti kulephela kumabweletsa kukula ku gulu lawo.
Kudziwilatu Kulephela kumabweletsa kukoma povomeleza zoikamo
Atsogoleri muutumiki amaphunzila kuchokela kwa Adamu ndi Eva kuti aziyembekezela kulephela, koyamba mwa iwo okha komanso mwa iwo amene amawatsogolela. Sakhala mu kulephela ndipo salimbikitsa kulephela. Koma amadziwilatu ndipo amatsogolera magulu awo ku chiyembekezo champhamvu choti kudzakhala kulephela mkati mwa ulendo. Amaphunzitsa magulu awo kulephela mwabwino, osati kukhala mbali chifukwa cholephela, komanso asakondwa ndi kulephela koma kuzindikila kulephelako. Amadalila mukulephela, ndi kupanga mapulani othana nako ndikuphunzilanso kuchokela mu kulephelamo! Polankhula za kulephela ndi kuchotsa kusalana mu gulu lawo, amatakasa kukoma ngakhale mudziko lophwasuka. Atsogoleri muutumiki sangalenge munda wa Eden, koma pomwe akuonelatu kulephela, amalenga dzikolapansi lokoma lomwe aliyense payekhapayekha ndi magulu amaphunzila kulimbikabe podutsa munjila yolephela.
Atsogoleri muutumiki mopitilila amaika mu utumiki wawo zofunika zonse kuti dziko likometsedwe. Ndipo zotsatila zingathe kuoneka mwa anthu omwe awazungulira omwe akukhala moyo okoma. |