Mbali imodzi ya dziko la Mulungu lokoma linali nyama zosiyanasiyana. Mwachangu Mulungu akumpatsa Adamu ntchito yoti achite yokhudzana ndi mbali ya nyama.
Genesis 2
19 Kenaka Yehova Mulungu anawumba ndi dothi nyama zonse zakuthengo ndi mbalame zonse zamlengalenga. Ndipo Iye anapita nazo kwa munthu uja kuti akazipatse mayina; ndipo dzina lililonse limene Adamu anapereka ku chamoyo chilichonse, lomwelo linakhala dzina lake.
20 Choncho Adamu anazitcha mayina ziweto zonse, mbalame zamlengalenga ndi nyama zakuthengo zonse. Komabe munthu uja analibe mnzake womuthandiza.
Ntchito yomwe Mulungu anampatsa Adamu ndi yofunika munjila zosiyanasiyana. Ikumupanga kukhala osiyanitsidwa ndi nyama ndipo ikumukonzela malo oti Mulungu amulengele okhala naye omuyenela. Zikuonetsela chiyembekezo cha Mulungu choti Adamu sanali ongoima padela chabe; amayenela kulamulira pa zolengedwa zonse. Ntchito imeneyi ikuonetsela kuti Mulungu amayembekezela kuti Adamu akule ndi kutukuka. Panali ntchito yoti agwile ndipo Mulungu amayembekezela kuti Adamu aphunzile ndi kupita patsogolo. Ophunzila ndi a sayansi amatsutsana pa nambala yeniyeni ya nyama zomwe Adamu ankafunika kuti azipatse maina ndipo sikuti amayenela kutchula maina a nyama zonse zomwe ndi za mitundu yosiyana siyana yokwana 1.2 miliyoni zomwe zili pa dziko lapansi. Komabe, ntchitoyo sinali yophweka yotenga nthawi ndi maola ochepa ayi! Atsogoleri muutumiki amaonetsetsa kuti chiyembekezo chokula chakhala chofunikila chokometsela dzikolapansi.
Kuyembekezela kukula kumabweletsa kukoma pozindikila cholinga
Mulungu akubweletsa nyama kwa Adamu ndipo ankayembekeza Adamu kuti azipatse Mulungu analenga Adamu ndi kuthekela kopatsa maina nyama koma tsopano Adamu anayelela kuti akule nkuthekela kumeneko ndi kubwela ndi maina! Mulungu akadatha kupereka maina Kwa Adamu ndi kumuuza kuti aloweze koma ankafuna kuti Adamu akule. Kukula kumapangika mmagazi mwathu ndipo ndi choyembekezeka cha chilengedwe. Timakondwela ndi tiwana tikamaphunzila kuyenda koma timakhala ndi chiyembekezo kuti akule ndi kukhwima. Timayembekeza kupita patsogolo Kwa kuzindikila ndi kukhwima zomwe zimabwela pomwe ana akupita patsogolo kudzela munjila yophunzila. Ndipo chikonzero cha kukula ndi choyembekezeka kupitilira moyo wathu onse. Atsogoleri muutumiki amazindikira cholinga cha Mulungu choti munthu azikula.
Kuyembekezela kukula kumabweletsa kukoma powonelatu zotsatila
Mulungu akuyenela kuti anamwetulila pomuona Adamu akuganizila kenaka kutchula dzina! Ndipo analingalira dziko lodzala ndi amai komanso abambo aliyense akutakasuka ndinso akukula, akuphunzila ukadaulo wa ulamuliro.Koma zachisoni, anthu ambiri lero amangopezeka pantchito ndi cholinga choti alandile malipilo,osayembekezela kusintha ndi kukula. Amalowa mumpingo pongoyembekezela misonkhano ndi kutakasika mkati mwawo. Atsogoleri muutumiki amayang'ana pa iwo amene akuwatumikira ndipo posayang'ana chomwe ali lero chokha, koma kuona chomwe azakhale. Amaonelatu kukula komwe kukubwela pa ogwira ntchito kozakhala oyendetsa kampani kapena kuti manejala. Amayembekezela kuti membala watsopano azalule kukhala mtsogoleri wa nthawi yatsogolo. Amalota za bungwe lawo litadzadza ndi anthu ochitachita mwamphamvu, akuphunzila ndi kukula mukuthekela kwawo kowumba dziko lawo.
Kuyembekezela kukula kumabweletsa kukoma povomeleza zoikamo.
Atsogoleri muutumiki amazindikilanso kuti Mulungu waika iwo pamalo a utsogoleri kuti atakase ndondomeko ya kukula. Poyambilira amaonetsetsa kukula pa Iwo eni, kupitiliza kufunafuna kupita patsogolo ndi kuphunzila. Kenaka amazindikira kuti Mulungu anampatsa Adamu ntchito ndicholinga choti akule. Atsogoleri muutumiki amatenga udindo kuti awatumikile anthu omwe akuwatsogolera powapatsa ntchito zovuta zomwe zingatambasule kuthekela Kwa otsatira awo.Amalimbikitsa, amakhala kholo Kwa Iwo,mlangizi ophunzitsa ndi otsogolera ena kuti afike pa kuthekela kwawo kwathunthu. Ndipo,monga Mulungu akanachitira,amayang'ana ndi kumwetulira pankhope pawo chifukwa choti akhutira pomwe akuwona ena akukula ndi kuchitabwino pozungulira pawo. |