Mulungu analenga dzikolapansi lokongola lomwe linali lokoma,lamoyo ndi labwino magawo onse. Koma tsono, kwa nthawi yoyamba, chinachake chafotokozedwa kuti "sichinali bwino"Kwa nthawi yoyamba.
Genesis 2
18 Ndipo Yehova Mulungu anati, “Sibwino kuti munthu akhale yekha. Ndidzamupangira mnzake womuthandiza.”
Kodi chomwe "sichinali bwino" mudziko ndi chani? Munthu analengedwa mwa mtengo wapatali popeza analengedwa muchifanizo Cha Mulungu. Adamu anali bwino. Koma "sikunali" kwabwino kwa Iye kuti akhale yekha. Analengedwa kuti akhale pa maubale ndi ena. Kawirikawiri timaona izi kuzela pa ubale wa ukwati chifukwa Mulungu analenga mkazi kuti akwanilitse chosowa chamamuna. Koma chimalozelanso pa chinachake chozamilako mu chikonzero cha Mulungu, chosowa chathu cha maubale. Mulungu anali ndicholinga poonetsetsa kuti tizindikile chokometsela Ichi cha dzikolapansi lokoma povomeleza chimodzi chomwe sichinali bwino, munthu kukhala yekha! Atsogoleri muutumiki amalingalira pa pulani ya Mulungu yolemekeza maubale ngati mbali ya dziko lapansi Lake lokoma.
Kulemekeza maubale kumabweletsa kukoma pozindikila cholinga
Cholinga cha Mulungu chinali choti maubale ndi ena kukhale chopangitsa munthu kukhala munthu. Mamuna oyamba ndi mkazi oyamba anabweletsedwa pamodzi muubale komanso pamodzi muubale ndi Mulungu. Anakonza kuti ife tikhale, tigwilentchito, komanso tiyende pamodzi ndi ena. Ngakhale munthu yemwe amakhala kwambili moyo wayekha amafunabe ena! Sichodabwitsa kuti kutsekeledwa kwawekha kimatengedwa kukhala chilango chachikulu kapena chizunzo. Sitinalengedwe kuti tikhale tokha! Cholinga cha Mulungu chinali choti wina aliyense wa ife apeze tanthauzo, kufunikila,ndi cholinga Kwa ena. Mumabanja omwe tinachokela, anakonza maubale omwe umatipangitsa kudziwika, ndinso kukhala a mubanjamo, ndi owelengedwa. Pomwe tikukhala muubale ndi ena, timatha kumanga kuthekela kozama muubale komwe mumabweletsa chimwemwe ndi tanthauzo kuzomwe timapanga.
Kulemekeza maubale kumabweletsa kukoma povomeleza zotsatila
Tchimo limabweletsa kuwawa kwakukulu ndi kuphwasuka kwa maubale zomwe ambiri amati zikanakhala bwino kumakhala wekha.Ndipo zikhalidwe zina zimalemekeza kukhala moyo wawekha kusiyana ndi moyo odalilana. Koma atsogoleri muutumiki amazindikira kuti kulemekeza maubale ndi mbali imodzi yolemekeza chikonzero cha Mulungu. Amaona mabizine awo, mpingo, banja, ndi mudzi ngati Malo omwe Mulungu amafuna anthu akhale ndi maubale amphamvu ndi abwino. Amangala ndi masomphenya a dzikolapansi lomwe magulu amphamvu amagwila ntchito limodzi mwamgwilizano kuti akwanilitse zinthu zazikulu.
Kulemekeza maubale kumabweletsa kukoma povomeleza zoikamo
Atsogoleri muutumiki amazindikira kuti pali zoikamo zambiri za utsogoleri kuti maubale alemekezedwe. Choyamba, amasakasaka kulowa ndi kusunga maubale amphamvu ndi abwino a wina ndi mzake. Amasakasaka maubale okazikika ndipo amakana mayeselo oti azikhala pamalo paokha. Kenaka amafuna kutsogolela omwe amawatumikila kuti azikhala pa maubale abwino. Amapanga magulu ndikuwatsogolela ku ndondomeko yozindikila momwe angayendetsele mofanana chilungamo ndi kukomamtima. Amafufuza munthu yemwe amaikidwa kumbali ndi kufunafuna kuwabweletsa mugulu. Amalimbikitsa anthu omwe ndi a chete kuti alankhule ndi kupeza cholankhula. Atsogoleli muutumiki amazindikira kuti kukwanilitsa Kwa masomphenya kumachitika pokhapokha ngati maubale Alemekezedwa. Choncho, amalimbikitsa nthawi osati yongokwanilitsa ntchito kokha komanso yomanga maubale. Atsogoleri muutumiki amafuna zotsatila, koma sanyozela maubale. Amapanga malo omwe anthu amakhala mokoma pamodzi mu maubale amphamvu ndi abwino. Atsogoleri muutumiki amapanga dziko lapansi lokoma pozungulira pawo polemekeza maubale.
|