Chokometsela choyamba mu dzikolapansi lokoma ndichoti anthu ndi a mtengo wopambana zonse. Mulungu analenga dziko labwino zedi,lodzala ndi nyama, zomela ndi lokongola modabwitsa. Zolengedwa zonse zinali zamtengo wake. Koma anthu omwe analenga anali ndi mtengo oposa.
Genesis 1
26 Zitatha izi Mulungu anati, “Tipange munthu mʼchifanizo chathu, mofanana ndi ife kuti alamulire nsomba za mʼnyanja, mbalame zamlengalenga, nyama zonse zoweta ndi zonse zokwawa za pa dziko lapansi ndi zamoyo zonse zakutchire.”
Chikonzero cha Mulungu anaika anthu kukhala osiyana ndi nyama zonse ndipo amawapatsa malo a ulamuliro pa chilengedwe chonse. Kupambana koma anaika pa anthu kunapanga dzikolapansi lokoma ndipo ndipo atsogoleri amalingalira mozama pa momwe kulemekeza anthu kumapambanitsila utsogoleri wawo.
Kuona kufunika kwa anthu kumabweletsa kukoma pa dziko lapansi pozindikila cholinga chawo.
Buku la Genesis likutionetsela cholinga chenicheni cha Mulungu pomwe analenga anthu. "Tipange munthu m'chifanizo chathu...." Analenga anthu muchifanizo cha Iye mwini nkuikamo umulungu. Ngakhale mitundu yamabuku onse sangafotokoze ndi kumaliza cholinga cha Mulungu. Koma Mulungu anaika anthu pa mulingo opambana kukongola kwa chilengedwe chake chonse ndi kuwapatsa zoyeneleza komanso cholinga. Chifanizo za Mulungu chikuonekela pa kuthekela kopanga zinthu mwa anthu, kutha kuweluza, kuthekela kokonda, kuthekela kokhala ndi masomphenya ndi mapulani, ndi kulumikizana. Mtengo wawo ndi mbali ya chomwe ali, sikuti chifukwa ndi anthu chabe ayi, kapena kuthekela kocholukana kokha ayi. Ali ndi mtengo wapatali chifukwa ndi anthu! Atsogoleri omwe amayang'ana pa anthu awo ndi kuwelengela phindu lomwe amabweretsa lokha mugulu lawo amasiya mtengo wapatali wa iwo monga anthu. Atsogoleri muutumiki amayang'ana pa anthu ndi kuwona chifanizo cha Mulungu mwa wina aliyense. Amaona kuthekela ndi kufunikila Kwa wina aliyense posatengela mmene aliri kapena udindo wawo.
Kuona kufunika Kwa anthu kumabweletsa kukoma pa dziko lapansi powona phindu.
Kodi dziko lapansi lingawoneke bwanji ngati wina aliyense awoneka ofunika ndi wamtengo wapadeladela monga mwa cholinga cha Mulungu? Atsogoleri muutumiki amakhala ndi masomphenya a dziko lomwe anthu amatulitsa zabwino zili mwaiwo kuti zigwire ntchito tsiku ndi tsiku, azigwilitse ntchito kwathunthu, akhale ndikufuna kochoka pansi pamtima pawo pa zomwe akuchita, kuganizira njira zopititsila mtsogolo, atulutse mopanda mantha maganizo awo payekha payekha, ndi kutha kuwunika bwino zinthu kuti apange chisankho. Tingathe kuona phindu losowa ndi kuthekela komwe kungabwele pa bungwe ngakhale limodzi lokha lomwe izi zakhala zenizeni. Ndipo Kodi mmudzi mungaoneke bwanji momwe munali ma kampani ambiri, ma tchalitchi ndi nyumba omwe amawelengela ndi kulemekeza umunthu wa anthu zeni zeni? Atsogoleri muutumiki amakhala mu masomphenya a dzikolapansili ndi kutsogolera munjira zomwe zimalika anthu kukhala a mtengo wapatali kuposa phindu kapena zomwe akubweletsa. Atsogoleri muutumiki amaganizila kuti mpingo wawo kapena bizinesi yawo zikhala malo omwe anthu akuwatenga kukhala a mtengo wapatali monga Mulungu anakonzela kuyambila pa chiyambi ndipo amaona zotsatila zabwino zosefukila mmabanja ndi mmaiko.
Kuona kufunika kwa anthu kumabweletsa kukoma pa dziko lapansi povomeleza zoikamo.
Atsogoleri muutumiki amavomereza kufunika kolemekeza anthu ndipo choyamba amafunafuna kukhala muchimenechi Iwo pokhala atsogoleri. Amaima ndi kulankhula ndi munthu yemwe akukolopa. Amadziwa anthu omwe akuwatsogolera ngati anthu eni eni omwe ali ndi maina, mabanja, ana komanso maloto. Amalimbikitsa anthu kukhala kupanga zinthu zatsopano ndipo amavumbulutsa kuthekela komwe kuli mwa munthu aliyense. Atsogoleri potumikila amakhala ofuna kupereka dipo lopanga hayala ogwira ntchito yemwe wakhala akukanidwa mmaso mwa anthu chifukwa amaona kufunika komwe kuli mwa munthu aliyense. Atsogoleri muutumiki amalenga dzikolapansi lokoma powazungilira polemekeza anthu. |