|
Atsogoleri Odzidalira Amalimbikitsa
Gawo #366, May 6, 2026
Mu phunziro lapitali tinaona momwe Yesu analili mtsogoleri odzidalira chifukwa ankadziwa ulamuliro Wake, chomwe anali komanso tsogolo. Kudzidalira kwake kunamuyeneleza iye kutumikila ophunzila ake. Tsopano, tiona njira zingapo momwe atsogoleri odzidalira amatumikilira omwe amawatsogolera- çhoyamba polimbikitsa. Nkhani ya Barnaba imatipatsa ife chithunzi chokongola cha mtsogoleri odzidalira muutumiki, zomwe anazionetsela muchilimbikitso chake. Dzina lake linkatanthauza"Mwana wa chilimbikitso"(Onani Machitidwe 4: 36) ndipo chimodzi mwa ntchito zake chinali kulimbikitsa mpingo ku Yerusalemu kuti amulandile otembenuka watsopano Saulo. Kenaka, atsogoleri ku Yerusalemu anamutuma kuti akagwire ntchito yofunika ku mpingo watsopano ku Antiokea.
Mbiri imeneyi inamveka ku mpingo wa ku Yerusalemu ndipo iwo anatumiza Barnaba ku Antiokeya. Atafika ndi kuona chisomo cha Mulungu pa iwo, anakondwa ndi kuwalimbikitsa anthu onsewo kuti apitirire kukhala woona mu mtima mwa Ambuye. Barnabayo anali munthu wabwino, wodzazidwa ndi Mzimu Woyera ndi chikhulupiriro ndipo gulu lalikulu la anthu linabwera kwa Ambuye.
Kenaka Barnaba anapita ku Tarisisi kukafuna Saulo, ndipo pamene anamupeza anabwera naye ku Antiokeya.
Machitidwe A Atumwi 11: 22-26a
Barnaba anafika pa mpingo wake watsopano ndi "kuwalimbikitsa. "Titha kuphunzira kuchokera pa chitsanzo chake chifukwa chomwe atsogoleri odzidalira amalimbikitsira bwino ena.
Atsogoleri odzidalira amalimbikitsa chifukwa amaika chidwi pa ena
Barnaba anapita ku Antiokea ndipo anaona "zomwe chisomo cha Mulungu chinachita"mu miyoyo ya omwe anali mumpingo. Anaika chidwi pa iwo, osati pa iyemwini. Sanayesele kuonetsa kufunika kwake ndi kuzionetsela zomuyeneleza zomwe zinamubweletsa ku Antiokea. Mmalo mwake, anaika chidwi chake pa omwe akanawatumikira. Atsogoleri osadzidalira sangachite zinthu za ena ;dziko lawo limazungulira pamodzi modzi pa zoti akwanilise, pazokhumba zawo, ndi pazolinga zawo. Amafuna ena apange za iwo. Koma atsogoleri odzidalira amazindikira kuti utsogoleri wawo si wokhudzana ndi iwo, koma ena. Amakwanitsa kuika chidwi pa omwe amawatumikira.
Atsogoleri odzidalira amalimbikitsa chifukwa amasangalala ndi ena
Barnaba anafika ndipo anaona chizindikiro chochitabwino mmoyo wawo. Ankadziwa kuti " anali munthu wabwino"koma odzidalira mokwana kuti akhale 'okondwa' kuona ena akuchita bwino. Atsogoleri osazidalira sakhala ndi chitsimikizo cha kuthekela kwawo kotero amadalira ena kuti zawo zikwanilitsidwe ndi kupangitsa zawo ziziyendabwino. Amagwira ntchito molimbika kuti asangalatse ena ndi kulabadila zoti akwanilitse zinthu zawo. Amakonda kumva owatsatira akunena za ubwino wao ndipo amafuna ena asangalale ndi iwo. Koma atsogoleri odzidalira amakhala otsimikizika muntchito zawo ndipo amayang'ana pa kuchitabwino kwa ena ndi kusangalala nawo pamozi. Amatumikira polimbikitsa kuchitabwino mwa ena.
Atsogoleri odzidalira amalimbikitsa chifukwa amaona kufunika kwa ena
Barnaba sanangolimbikitsa okhulupilira a ku Antiokea okha, koma anamufufuzanso Paulo kuti abwele azathandizane ntchito. Analemekeza ntchito ya uphunzitsi yomwe Paulo akadabweletsa kugulu lawo ndipo samaophyedwa ndi mphatso yake. Anali odzidalira mukufunika kwa iye mwini ndichifukwa amatha kuona kufunika kwa ena. Atsogoleri osadzidalira sakhala otsimikizika mu kuthekela kwawo ndi maitanidwe awo, kotero amachita mpikisano ndi ena mukuyesetsa kwawo kuti afikile pamwamba ndikuti awonetse kufunika kwawo. Amaona mphatso za ena ngati chiophyezo kwa iwo. Koma atsogoleri odzidalira amadziwa kuti iwo ndi ndani, moonamtima amavomeleza zomwe sakwanitsa ndi zomwe amakwanitsa. Sanakhale pa utsogoleri kuti akankhile ena pansi kapena kuonetsela kuti iwowo ndiabwino motani. Amalemekeza mphatso za ena ndi kutumikila polimbikitsa mphatso zonse pagulu.
Zoti tilingalire ndi kukambilana
- Kodi omwe andizungulira angandifotokoze ngati munthu yemwe ndimawalimbikitsa? ( ngati simungatsimikize, afunseni!) Kodi moyo wa Barnaba ukundibetchela motani kuti ndikule mudela lolimbikitsa?
- Kodi utsogoleri wanga ndi chindunji pa ine ndekha motani ndipo pa ena chidwi chake nchotani? Kodi ndingachite chani lero pa ine mwini ndi kulimbikitsa wina wa pagulu langa?
- Kodi pomwe ena akuchita bwino, Kodi ine ndimamvabwanji - kusangalala kapena kukhala ndi nsanje? Lingalirani pa chitsanzo chongochitika posachedwapa chomwe winawake anapanga bwino ndipo anayamikidwa chifukwa cha chimenechi. Unguzani mayankho anu. Munjila yanji imene yankho lanu likukhudzila utsogoleri wanu?
- Kodi ndimunjila yanji imene ndimalemekezela mphatso za ena a mugulu langa? Kodi ndingachite chani lero kuti ndizindikile komanso kulimbikitsa mphatso ya mzanga kapena yemwe ndilinaye mugulu?
Muphunziro lotsatilari, tiona momwe atsogoleri odzidalira amapelekela ntchito kwa ena.
|