Tiyeni Tilankhule Zandalama: Pelekani

Gawo #364, March 11 , 2026

Mbuyomu tinaona kuti atsogoleri muutumiki amaziona kuti iwo ndi ongosunga chabe ndalama ndipo amalingalira za momwe amapezela ndalama. Ndi maziko amenewa, mtima wa atsogoleri muutumiki umaonekela kwatunthu pomwe amapeleka mowolowamanja chuma chawo ndi ena. Atsogoleri muutumiki amakhala moyo wawo onse ndi cholinga chawo pa ena ndipo izi zimaonekela pogawana ndi wena. Mtima wopeleka umenewu umaumbidwa ndi mavesi ngati otsatilawa:  

Pa zonse zimene ndinachita,  ndinakuonetsani kuti pogwira ntchito molimbika motere tiyenera kuthandiza ofowoka,  pokumbukira mawu a Ambuye Yesu akuti,  “Kupereka kumadalitsa kuposa kulandira. ” (Machitidwe 20: 35) 

Munthu aliyense apereke chimene watsimikiza mu mtima mwake kuti apereka,  osati monyinyirika kapena mokakamizidwa,  pakuti Mulungu amakonda wopereka mokondwera. (2 Akorinto 9: 7) 

Ndipo tsopano,  abale,  tikufuna kuti mudziwe za chisomo chimene Mulungu wapereka ku mipingo ya ku Makedoniya. Pakati pa mayesero owawitsa,  chimwemwe chawo chosefukira ndi umphawi wawo otheratu,  anapereka mowolowamanja kwambiri. (2 Akorinto 8: 1-2) 

Kupereka kumaonetsela mtima omwe uli chidwi pa kutumikila ena mmalo mwa iwemwini. Atsogoleri muutumiki amatsegula mitima yawo kwa omwe amawatumikira  munjira zambiri. Muzachuma chidwi cha pa enachi chimaonetseledwa mu kupeleka molowamanja.

Atsogoleri muutumiki amapereka mwadongosolo

 "Kupereka kumadalitsa kuposa kulandira." Mau a Yesu akutikumbhutsa kuti ndidalitso lokulirapo popeleka kuposa kulandira. Atsogoleri ena amangopeleka chabe pakakhala chosowa chamsangamsanga ndi kuiwala za kupereka nthawi zina. Opanda kusintha, amakhala ndi chidwi  kwambiri popeza ndalama kuposa pa kupereka. Koma atsogoleri muutumiki amakhala ndi malingaliro ndiponso cholinga chopereka. Amasakasaka njira zomwe angapelekere,  malo komwe angapeleke, anthu omwe  angawadalitse. Amaima ndi kulingalira za zomwe amapereka ndi momwe angachulukitsile mapelekedwe awo. Amakhala ndicholinga.

Chifukwa ndi ongosunga chabe atsogoleri muutumiki amafunafuna kupereka munjira zomwe zimafanana ndi mtima wa mwiniwake weniweni wa zinthu,  Mulungu!Amapemphera kawilikawili za momwe ndi komwe angapeleke. Amazindikira kuti pomwe kupereka nthawi zonse kumadalitsa yemwe amapereka,  nthawi zina zitha kukhala ndi zotsatira zosayembekezeka kwa olandilayo. Kotero amayang'ana njira zoti angathandizire omwe ali ndi zosowa munjira zomwe zimalimbikitsa ndi kudalitsa. Amafufuza mosamala mabungwe omwe akubweletsa zotsatira zogwilika ndi kuwapatsa thandizo. Atsogoleri muutumiki amazindikira kuti kupereka kwenikweni kobweletsa zotsatila kumachitika popeleka mwadongosolo.

Atsogoleri muutumiki amapereka ndalama ndi msangala

"Mulungu amakonda opereka mokondwera.” Sionse omwe amapereka amatero ndi Chimwemwe. Atsogoleri ena, amamva kukakamizidwa kupereka kapena kuopa kutsutsika pakusapereka kapena akufuna kuti awoneke ndi ena kuti ndiopereka, koma mtima wawo suli muzimenezo. Koma atsogoleri muutumiki amakonda kupereka ndipo amampanga izi mokondwera! Omwe amapereka ndi anthu omwe ndi osangalala kupezeka pamalo ndipo atsogoleri muutumiki ndi okondwa pakugawa.

Atsogoleri muutumiki amapereka ndalama ndicholinga chachitsanzo

Atsogoleri omwe akumana ndi  dalitso komanso chimwemwe pa kupereka mwachiziwikile amafuna enanso kuti akumane ndi zotero. Kotero,  atsogoleri muutumiki amapereka ndalama kuti awonetsele kwa ena momwe angakhalire ndi mtima wopereka. Samapereka kuti apange chionetsero,  koma amapereka kuti akhudze ena kuti nawonso akhale opereka. Monga mpingo wa ku Makedonia, unakhala chitsanzo cha kupereka kwa ena. Mtsogoleri muutumiki yemwe ndinamuyendela posachedwapa anandiuza kuti chimodzi mwa cholinga cha kampani yawo ndi kuikiza mzimu wopeleka pakati pa ogwira ntchito awo. Umenewo nde mtima wa utsogoleri muutumiki, ofuna ena kuti nawonso apeze  chimwemwe ndi dalitso la kupereka.

Zoti tilingalire ndi kukambirana 

  •  Muzipatse nokha "kafukufuku opereka" polingalira pa mafunso awa:
    •  Kodi ndimalingalira mochuluka motani pa momwe ndingapelekere  kwambiri, momwe ndingapelekere mwanzeru, momwe ndingapelekere mwachimwemwe chochuluka?
    • Kodi muyeso wanga wakupereka mwaukadziotche ukuchuluka kapena ukuchepa?
    •  Kodi ndimapereka mowilingula kapena mosafuna?
    • Kodi banja langa ndi omwe andizungulira amandiona kuti ndine opereka kapena ongotenga?
  • Kodi ndingachite chani kuti ndizipereka kuchoka pansi pamtima?
  •  Kodi ndingalimbikitse bwanji omwe ndimawatumikira kuti akhale opereka mowolowamanja?
  •  Onani mavesi otsatilawa okhudzana ndi kupereka: (Miyambo 3: 9-10, 11: 25, 22: 9, 28: 7, 22; Luka 6: 38, ndi 2 Akorinto 8: 1-7) Kodi mukuphunilapo zinthu zina zotani zokhudzana ndi kupereka kuchokera mmavesi amenewa?

Kufikira nthawi ina, Ine wanu wa paulendo,

Jon Byler

Kuti mulandile izi pa WhatsApp dinani apa

 

Kuti muone maphunziro a m'buyomu, dinani apa.

Tumizani kwa anzanu omwe akufuna kutsatila chitsanzo cha Yesu potsogolera ngati otumikira. Angathe kulembetsa mwaulere komanso kuona magawo akale.mukafuna kupeza magawo akale, dinani apa. Magawo awa amatanthauziridwa mchichewa ndi abusa Grace Kacheto, gracekacheto@yahoo.com

Reflections for Serving Leaders is published by Leaders Serve and Jon Byler. Copyright, 2026

Unsubscribe   |   Modify your subscription   |   View online