Okondedwa Mzanga,
Munthawi ino ndikukufunilani chikondwelero chopambana Cha Christmas!
Pomwe mukulingalira kuti kubwela kwa Yesu kumatanthauzanji kumoyo wanu pemphelo langa ndi loti Mulungu akupatseni mphamvu kuti mupitilize kukula ngati mtsogoleri muutumiki.
Yesaya ananenela za zomwe zizachitike kudzela mukubadwa kwa Yesu.
Yesaya 9
2 Anthu oyenda mu mdima awona kuwala kwakukulu; kwa iwo okhala mΚΌdziko la mdima wandiweyani kuwunika kwawafikira.
Anabwela kuzapeleka kuwala kudziko lathu,kutionetsela kwatunthu njila yatsopano ya kukhala,kukonda ndi kutsogolera.Anabweletsa kuwala ku utsogoleri potumikila ena.
Dziko lathu likufunika kuwala Kwake! Ndipo pomwe Inu ndi ine tikutsatila utsogoleri otumikila ,tikufalitsa kuwala Kwake mmakomo mwathu,mmadela,mmabungwe ndi mmaiko.
Pitilizani kuwala Kwa Iye!
Zikomo chifukwa cha chikhumbokhumbo chanu chofuna kuwelenga ziphunzitso zimenezi ndikukula nane pamodzi pa maulendo athu autsogoleri! Mundifikile ine ngati muli ndi maganizo othandiza kuti tichitebwino kuposa apa.
Pakutha kwa chaka chino, ndikufuna kuti ndithokozenso omwe amagwira ntchito kuti Inu muzilandila izi.Linda Boll amawelenga ndikukonza pena ndi pena phunziro liri lonse ndi Brian Drewery yemwe amapangitsa zida zamakonozi kutheka. Gabriel Mandrazo yemwe amamasulira izi kupita ku chiyankhulo Cha Spanish. Grace Kacheto Banda yemwe amakumasulirani mchichewa ndipo ndili othokoza kwambili chifukwa cha ntchito yake. Ngati mungafune kumuthokoza panokha chonde muimbileni pa +265 884 82 19 37 |